1 Kings 9:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiponso mizinda yonse yosungiramo chuma chake ndi magaleta ake, mizinda ya anthu ake okwera pa akavalo, ndiponso chilichonse chimene Solomoniyo ankafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku maiko onse amene iye ankalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi midzi yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi midzi yosungamo magaleta ake, ndi midzi yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamodzinso ndi mizinda yake yosungira chuma ndiponso mizinda yosungiramo magaleta ndi akavalo ake. Anamanganso chilichonse chimene anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi midzi yonse yosungamo zinthu zace za Solomo, ndi midzi yosungamo magareta ace, ndi midzi yokhalamo apakavalo ace, ndi zina ziti zonse zidakomera Solomo kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.