1 Kings 9:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiye kuti zidzukulu zao zotsalira m'dzikomo. Onsewo zimene Aisraele sadathe kuŵaononga kotheratu. Anthu ameneŵa Solomoni ankaŵagwiritsa ntchito yathangata, ndipo akugwirabe ntchito imeneyo mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a lsrayeli sanakhoza kuononga konse, Solomo anawasenzetsa msonkho wa nchito kufikira lero.