1 Kings 9:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Aisraele Solomoni sankaŵagwiritsa ntchito yaukapolo. Iwowo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri ankhondo, olamulira ocheperapo a ankhondo, ndiponso oyang'anira magaleta ake, ndi anthu ake okwera pa akavalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Solomoni sanawayese ana a Israele akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi akazembe ake, ndi oyang'anira magaleta ake ndi apakavalo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Mwisraeli aliyense; iwo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri a ankhondo, akapitawo ake, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Solomo sanawayesa ana a Israyeli akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi akazembe ace, ndi oyang'anira magareta ace ndi apakavalo ace.