1 Kings 9:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo mwana wamkazi wa Farao adachoka ku mzinda wa Davide napita ku nyumba yake imene Solomoni adammangira. Pambuyo pake Solomoni adamanga linga la Milo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mudzi wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wamkazi wa Farao atachoka mu Mzinda wa Davide, kupita ku nyumba ya mfumu imene Solomoni anamumangira, Solomoni anamanga malo achitetezo a Milo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mwana wamkazi wa Farao anaturuka m'mudzi wa Davide kukwera ku nyumba yace adammangira Solomo, pamenepo iye anamanganso Milo.