1 Kings 9:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mfumu Hiramu adatumiza zombo zake pamodzi ndi atumiki ake, ndiye kuti amalinyero odziŵa zam'nyanja, kukagwira ntchito pamodzi ndi anthu a Solomoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ake m'zombozo amalinyero ozolowera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Hiramu anatumiza anthu ake oyendetsa sitima zapamadzi amene ankadziwa za pa nyanja kuti aziyendetsa pamodzi ndi anthu a Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ace m'zombozo amarinyero ozerewera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomo.