1 Kings 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo ndidzaŵachotsa Aisraelewo m'dziko limene ndidaŵapatsa. Ndipo Nyumba ino imene ndaipatulira dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga. Motero Aisraele adzasanduka ngati mwambi ndi chisudzo chabe pakati pa anthu a mitundu yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko limene ndinawapatsa ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndayipatula chifukwa cha Dzina langa. Pamenepo Aisraeli adzasanduka mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo Ine ndidzalikha Aisrayeli kuwacotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israyeli adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.