1 Kings 9:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumba yotchuka ndi yokomayi idzasanduka bwinja, ndipo aliyense wopitapo adzadabwa nadzaimba likhweru, nkumafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta walichita zotere dzikoli ndiponso Nyumbayi?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero chifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzatsonya ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero cifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?