1 Peter 1:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndine, Petro, mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa inu osankhidwa a Mulungu, amene muli obalalikira ku chilendo, ku maiko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya ndi Bitiniya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndine Petro, mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa onse osankhidwa ndi Mulungu, alendo mʼdziko lapansi, obalalikira ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya ndi Bituniya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
PETRO, mtumwi wa Yesu Kristu, kwa osankhidwa akukhala: alendo a cibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,