1 Peter 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adaŵaululira kuti ntchito yaoyi sankaigwira chifukwa cha eniakewo, koma chifukwa cha inu, pamene iwo ankanena zoonazi zimene mwamva tsopano. Olalika Uthenga Wabwino adakuuzani zoonazi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera Kumwamba. Angelo omwe amalakalaka kuwona nao zinthuzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kucokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.