1 Peter 1:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo Mulungu adaamsankhiratu dziko lapansi lisanalengedwe, koma wamuwonetsa nthaŵi yotsiriza ino chifukwa cha inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anasankhidwa lisanalengedwe dziko lapansi, koma waonetsedwa chifukwa cha inu pa nthawi ino yotsiriza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
3 amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa citsiriziro ca nthawi,