1 Peter 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa namupatsa ulemerero. Nʼchifukwa chake chikhulupiriro ndi chiyembekezo chanu chili mwa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa ca inu amene mwa rye mukhulupirira Mulungu 4 wakwnuukitsa iye kwa akufa, ndi kumpatsa iye ulemerero; kotero kuti cikhulupiriro canu ndi ciyembekezo canu cikhale pa Mulungu.