1 Peter 2:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu ndi chinthu chabwino ngati munthu, chifukwa chokumbukira Mulungu, apirira zoŵaŵa zosamuyenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ici ndi cisomo ngati munthu, cifukwa ca cikumbu mtima pa Mulungu alola zacisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.