1 Peter 2:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi pali chiyani choti nkukuyamikirani ngati mupirira pamene akumenyani chifukwa choti mwachimwa? Koma mukapirira zoŵaŵa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pocimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pocita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko cisomo pa Mulungu.