1 Peter 2:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
6 amene anasenza macimo athu mwini yekha m'thupi mwace pamtanda, kuti ife, 7 titafa kumacimo, tikakhale ndi moyo kutsata cilungamo; 8 ameneyo mikwingwirima yace munaciritsidwa nayo.