1 Peter 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kwa inu okhulupirira, Iye ndi wamtengowapatali. Koma kwa osakhulupirira, ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Mwala womwe amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa inu tsono akukhulupirira, ali wa mtengo wake; koma kwa iwo osakhulupirira, Mwala umene omangawo anaukana, womwewo unayesedwa mutu wa pangodya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira, “Mwala umene amisiri anawukana wasanduka mwala wa maziko,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa inu tsono akukhulupira, ali wa mtengo wace; koma kwa iwo osakhulupira, Mwala umene omangawo anaukana, Womwewo unayesedwa mutu wa pangondya;