1 Peter 2:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa;