1 Peter 3:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo. Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, Ndi makutu ace akumva rembedzo lao; Koma nkhope ya Ambuye iri pa ocita zoipa,