1 Peter 3:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mumpatulikitse Ambuye Kristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kucita codzikanira pa yense wakukufunsani cifukwa ca ciyembekezo ciri mwa inu, komatu ndi cifatsondi mantha;