1 Peter 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kukhala nacho chikumbu mtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Khristu akachitidwe manyazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kukhala naco cikumbu mtima cabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Kristu akacitidwe manyazi.