1 Peter 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma woparsidwa moyo mumzimu;