1 Peter 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa cidziwitso, ndi kucitira mkazi ulemu, monga cotengera cocepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa cisomo ca moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.