1 Peter 3:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
osabwezera coipa ndi coipa, kapena cipongwe ndi cipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ici mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.