1 Peter 4:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti Khristu adamva zoŵaŵa m'thupi mwake, valani dzilimbe ndi maganizo omwewo, chifukwa munthu amene wamva zoŵaŵa m'thupi mwake, ndiye kuti walekana nawo machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Khristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo tchimo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Kristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo cimo;