1 Peter 4:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mau a Mulungu akuti, “Ngati wolungama yemwe adzapulumuka movutikira, nanga munthu wochimwa, wonyozera za Mulungu, adzatani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga Malemba akuti, “Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke, nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokha kokha, munthu wosapembedza ndi wocimwa adzaoneka kuti?