1 Peter 5:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kalatayi ndalembetsa Silivano mwachidule. Ndimamuwona kuti ndi mbale wokhulupirika. Ndafuna kukulimbitsani mtima, ndi kuchita umboni wakuti kukoma mtima kwenikweni kwa Mulungu nkumeneku. Chifukwa cha kukoma mtimako, limbikani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa Silvano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwacidule, ndi kudandaulira, ndi kucita umboni, kuti cisomo coona ca Mulungu ndi ici; m'cimeneci muimemo.