1 Samuel 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musayese kuti ine mdzakazi wanu ndine mkazi wachabechabe, pakuti nthaŵi yonseyi ndakhala ndikuulula kwa Chauta nkhaŵa yanga yaikulu ndi zovuta zanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; chifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kuchuluka kwa kudandaula kwanga ndi kuvutika kwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musaganize kuti mtumiki wanu ndi kukhala mkazi wachabechabe. Ine ndakhala ndi kupereka nkhawa yanga yayikulu ndi zowawa zanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; cifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kucuruka kwa kudandaula kwanga ndi kubvutika kwanga.