1 Samuel 1:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Hana sadapite nao chifukwa adaauza mwamuna wake kuti, “Malinga mwanayu akaleka kuyamwa, ndidzapita naye kuti ndikampereke kwa Chauta, ndipo adzakhala komweko moyo wake wonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Hana sadakwera, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Hana sanapite nawo popeza anawuza mwamuna wake kuti, “Mwanayu akadzaleka kuyamwa, ndidzapita naye ndi kukamupereka pamaso pa Yehova ndipo adzakhala kumeneko moyo wake wonse.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Hana sadakwera, cifukwa kuti anati kwa mwamuna wace, Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako cikhalire.