1 Samuel 1:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elikana mwamuna wake adamuuza kuti, “Uchite zimene zikukukomera, uyembekeze mpaka mwanayo ataleka kuyamwa. Kungoti Chauta achitedi monga momwe afunira.” Choncho mkaziyo adatsalira, namalera mwana wake uja mpaka atamletsa kuyamwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elikana mwamuna wake anati, Chita chimene chikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ake. Chomwecho mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wake, kufikira anamletsa kuyamwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elikana mwamuna wake anamuwuza kuti, “Chita chimene chakukomera. Tsala kuno mpaka utamusiyitsa kuyamwa, Yehova yekha akwaniritse mawu ake.” Choncho mkaziyo anatsala ku nyumba ndi kusamalira mwana wake mpaka atamuletsa kuyamwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elikana mwamuna wace anati, Cita cimene cikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ace. Comweco mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wace, kufikira anamletsa kuyamwa.