1 Samuel 1:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka ndi chaka Elikana ankapita ku Silo kuchokera ku mzinda kwao, kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Chauta Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, amene anali ansembe a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mudzi mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Mulungu wa makamu m'Silo. Ndipo pomwepo panali ana amuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chaka ndi chaka Elikana ankachoka ku mudzi kwawo kupita ku Silo kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Yehova Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi amene anali ansembe a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthuyu akakwera caka ndi caka kuturuka m'mudzi mwace kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Mulungu wa makamu m'Silo. Ndipo pomwepo panali ana amuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Pinehasi.