1 Samuel 1:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono chifukwa choti Chauta sadampatse ana, mkazi mnzake uja ankangomnyodola ndi kumpeputsa, kuti amkwiyitse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukulu, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukuru, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yace.