1 Samuel 1:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi zinkachitika chaka ndi chaka. Nthaŵi zonse akamapita ku nyumba ya Chauta, mkazi mnzakeyo ankamputa. Nchifukwa chake Hana ankangolira, ndipo sankafuna ndi kudya komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popeza munthuyo adatero caka ndi caka, popita mkaziyo ku nyumba ya Yehova, mnzaceyo amamputa; cifukwa cace iye analira misozi, nakana kudya.