1 Samuel 1:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwina Elikana mwamuna wake ankamufunsa kuti, “Hana, kodi watani apa ukulira ndi kuwoneka wachisoni ndiponso sukufuna kudya? Kodi kwa iwe ineyo sindikuposa ana aamuna khumi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwamuna wake Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mwamuna wake Elikana ankamufunsa kuti, “Hana ukulira chifukwa chiyani? Wakhumudwa ndi chiyani kuti sukufuna ndi kudya komwe? Kodi ine kwa iwe sindili woposa ana aamuna khumi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwamuna wace Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? ndipo umakaniranji kudya? ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindiri wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?