1 Samuel 1:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina iwo atatha kudya ku Silo kuja, Hana adaimirira nakapemphera. Nthaŵi imeneyo nkuti Eli, wansembe uja, ali pa mpando pambali pa khomo la Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wace pa mphuthu ya Kacisi wa Yehova.