1 Samuel 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Samuele adatenga nsupa ya mafuta nathira mafutawo pamutu pa Saulo. Ndipo adamumpsompsona nati, “Chauta akukudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu ake Aisraele. Udzalamulira anthu a Chauta ndi kuŵapulumutsa kwa adani oŵazungulira. Chizindikiro chakuti Chauta wakudzoza kuti ukhale mfumu yolamulira anthu ake, ndi ichi:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Samueli anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pace, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozani ndi Mulungu kodi, mukhale mfumu ya pa colowa cace?