1 Samuel 10:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene ankamdziŵa kale, ataona kuti akulosa limodzi ndi aneneri, adayamba kufunsana kuti, “Chamchitikira nchiyani mwana wa Kisi? Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene onse amene ankamudziwa kale anamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anafunsana wina ndi mnzake. “Kodi nʼchiyani chachitika ndi mwana wa Kisi? Kodi Sauli alinso mʼgulu la aneneri?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ici cakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzace, Ici nciani cinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulinso ali mwa aneneri?