1 Samuel 10:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wina wakomweko adayankhako nati, “Nanga enaŵa ndiye abambo ao ndani?” Nchifukwa chake padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Chifukwa chake mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulonso ali mwa aneneri?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Cifukwa cace mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulinso ali mwa aneneri?