1 Samuel 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbale wa bambo wake wa Saulo ataona Sauloyo ndi mnyamata uja, adaŵafunsa kuti, “Mudaapita kuti?” Saulo adayankha kuti, “Tidaakafunafuna abulu. Titaona kuti sakupezeka, tidaapita kwa Samuele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samuele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?” Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mbale wa atate wace wa Sauli ananena kwa iye ndi mnyamata wace, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna aburuwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samueli.