1 Samuel 10:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saulo adati, “Samuele adatiwuza bwino lomwe kuti abuluwo adapezeka.” Koma sadanene kanthu za nkhani ya ufumu ija imene Samuele adaamuuza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sauli anati kwa mbale wa atate wace, Anatiuza momveka kuti aburuwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitsa mau aja Samueli ananena zaufumuwo.