1 Samuel 10:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma lero lino, inu mwamkana Mulungu wanu amene amakupulumutsani m'mavuto anu onse ndi m'masautso anu. Mukuti, ‘Iyai! Koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Nchifukwa chake tsono musonkhane pamaso pa Chauta potsata mafuko anu ndi mabanja anu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Cifukwa cace tsono mudzionetse pamaso pa Mulungu mafuko mafuko, ndi magulu magulu.