1 Samuel 10:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja, ndipo pochita maere, banja la Matiri ndilo lidasankhidwa. Potsiriza pake adasonkhanitsa anthu a m'banja la Matiri mmodzimmodzi, ndipo pochita maere, Saulo mwana wa Kisi, ndiye adasankhidwa. Koma pamene adamfunafuna, sadampeze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayandikizitsa fuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Saulo mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayandikizitsa pfuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Sauli mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.