1 Samuel 10:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Samuele adafotokozera anthu zinthu zoyenera mfumu pa maudindo ake. Ndipo adazilemba m'buku nakaliika bukulo pa malo oyera pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Samuele adauza anthu kuti abwerere kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Samueli anafotokozera anthu macitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samueli anauza anthu onse amuke, yense ku nyumba yace,