1 Samuel 10:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu ena achabechabe adati, “Kodi munthu ameneyu angathe bwanji kutipulumutsa ife?” Ndipo adayamba kumnyoza Sauloyo, osampatsa ndi mphatso zomwe. Koma iye adangokhala chete.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala cete.