1 Samuel 10:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono utabzola pamenepo, ufika pa mtengo wogudira wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi anthu atatu, wina atanyamula anaambuzi atatu, wina atanyamula mitanda itatu ya buledi, ndipo wina atanyamula thumba lachikopa la vinyo, akupita kukapereka nsembe kwa Mulungu ku Betele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Beteli, wina wonyamula ana a mbuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.