1 Samuel 10:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzatsogola ndiwe kupita ku Giligala. Patapita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere. Kumeneko ndidzakulangiza zoti uchite.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono tsogola kupita ku Giligala. Ine ndidzabwera ndithu kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Koma ukandidikire masiku asanu ndi awiri mpaka ine nditabwera kuti ndidzakuwuze zomwe udzachite.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani cimene mudzacita.