1 Samuel 10:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Saulo adatembenuka kuti asiyane ndi Samuele, mtima wake Mulungu adausandutsa winawina. Ndipo zizindikiro zonse zija zidachitikadi tsiku limenelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samuele, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikiro zija zonse zinachitika tsiku lija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samueli, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikilo zija zonse zinacitika tsiku lija.