1 Samuel 11:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita ngati mwezi umodzi, Nahasi Mwamoni adanka ndi gulu lankhondo kukazinga mzinda wa Yabesi m'dziko la Giliyadi. Tsono anthu onse a mu mzinda wa Yabesi adapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe chipangano, ndipo tidzakutumikirani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nahasi, Mwamoni anapita ndi kuzungulira mzinda wa Yabesi Giliyadi. Tsono anthu onse a ku Yabesi anapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe pangano, ndipo tidzakutumikirani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Nahasi M-amoni anakwera, namanga Yabezi Gileadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabezi anati kwa Nahasi, Mupangane cipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu.