1 Samuel 11:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu a ku Yabesi adamuyankha kuti, “Mutiyembekeze masiku asanu ndi aŵiri, kuti titumize mithenga ku dziko lonse la Aisraele. Tsono ngati sipaoneka wina wotipulumutsa, pamenepo tidzadzipereka kwa inu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu a ku Yabesi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israele; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzatulukira kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu a mzinda wa Yabesi anati kwa iye, “Utipatse masiku asanu ndi awiri kuti titumize uthenga mu Israeli monse. Ngati sipapezeka wodzatipulumutsa, ndiye ife tidzadzipereka kwa iwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru a ku Yabezi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israyeli; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzaturukira kwa inu.