1 Samuel 11:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene amithenga adafika kwao kwa Saulo ku Gibea, nauza anthu nkhaniyo, onse adayamba kulira motaya mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono mithengayo inafika ku Gibea kwa Saulo, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amithenga aja atafika kwawo kwa Sauli ku Gibeya ndi kufotokoza nkhaniyi kwa anthu onse, iwo analira motaya mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono mithengayo inafika ku Gibeya kwa Sauli, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.