1 Samuel 11:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti Saulo akuchokera ku munda, akuyenda pambuyo pa ng'ombe zantchito. Tsono adafunsa kuti, “Chaŵavuta anthu nchiyani kuti azilira?” Pamenepo adamuuza nkhani ya anthu a ku Yabesi ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo, onani, Saulo anachokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Saulo, Choliritsa anthu misozi nchiyani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabesi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawiyo nʼkuti Sauli akubwera kuchokera ku munda, ali pambuyo pa ngʼombe zake za ntchito ndipo anafunsa. “Nʼchiyani chawavuta anthuwa kuti azilira motere?” Ndipo anamufotokozera zomwe anthu a mu mzinda wa Yabesi ananena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo, onani, Sauli anacokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Sauli, Coliritsa anthu misozi nciani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabezi.