1 Samuel 11:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa ng'ombe zija adapatulapo ziŵiri nazipha, ndipo adazidula nthulinthuli. Kenaka adatuma amithenga aja kuti akapereke nthulizo ku dziko lonse la Israele, ndi kumakanena kuti, “Umu ndimo m'mene adzaichitira ng'ombe ya aliyense amene sadzatsata Saulo ndi Samuele.” Apo anthuwo adagwidwa ndi mantha oopa Chauta ndipo onse adanyamuka ndi mtima umodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthulinthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israele, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Saulo ndi pa Samuele, adzatero nazo ng'ombe zake. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, natuluka ngati munthu mmodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anatenga ngʼombe ziwiri za ntchito, nazidula nthulinthuli. Ndipo anatumiza amithenga ndi nthulizo dziko lonse la Israeli ndi mawu akuti, “Umo ndi mmene adzachite ndi ngʼombe ya aliyense amene satsata Sauli ndi Samueli.” Ndipo anthu anachita mantha aakulu motero kuti onse ananyamuka ndi mtima umodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthuli nthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israyeli, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Sauli ndi pa Samueli, adzatero nazo ng'ombe zace. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, naturuka ngati munthu mmodzi.